2. Imvani ici, akulu akulu inu, nimuchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Cacitika ici masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?
3. Mufotokozere ana anu ici, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.
4. Cosiya cimbalanga, dzombe lidacidya; ndi cosiya dzombe, cirimamine adacidya; ndi cosiya cirimamine, anoni adacidya.
5. Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, cifukwa ca vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.
6. Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ace akunga mano a mkango, nukhala nao mano acibwano a mkango waukuru.
7. Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.
8. Lirani ngati namwali wodzimangira m'cuuno ciguduli, cifukwa ca mwamuna wa unamwali wace.
9. Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka ku nyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, acita maliro.
10. M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
11. Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; cifukwa ca tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
12. Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse ya kuthengo yafota; pakuti cimwemwe cathera ana a anthu.