Ndipo mfumu ya ku Ai, anampacika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wace pamtengo; ndipo anauponya polowera pa cipata ca mudzi; nauniikako mulu waukuru wamiyala, mpaka lero lino.