A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.