Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, kuti athawireko ali yense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.