1. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,
2. Nena ndi ana a Israyeli ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose,
3. kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalira inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.
4. Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.
5. Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.