6. ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;
7. Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;
8. ndi miraga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalata-beeri ndiwo Rama kumwera. Ndico colowa ca pfuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.
9. M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.
10. Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;
11. nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;
12. ndi kucokera ku Saridi anazungulira kumka kum'mawa kumaturukira dzuwa, mpaka malire a Kisilotu-tabori; naturuka kumka ku Daberati, nakwera ku Yafia;
13. ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,
14. nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;
15. ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.