5. Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Gileadi ndi Basana lokhala tsidya lija la Yordano:
6. popeza ana akazi a Manase adalandira colowa pakati pa ana ace amuna; ndi dziko la Gileadi linakhala la ana a Manase otsala.
7. Ndipo malire a Manase anayambira ku Aseri, kumka ku Mika-metatu, wokhala cakuno ca Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapua.
8. Dziko la Tapua linali la Manase; koma Tapua mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efraimu.
9. Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efraimu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndimaturukiro ace anali kunyanja;