Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.