Pakuti cidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisrayeli nkhondo kuti iye awaononge konse, kuti asawacitire cifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.