17. Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18. Atengedwa ngati coyandama pamadzi;Gawo lao litembereredwa padziko;Sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.
19. Cirala ndi dzuwa zitha madzi a cipale cofewa,Momwemo manda acita nao ocimwa.
20. M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera.Sadzamkumbukilanso;Ndipo cosalungama cidzatyoledwa ngati mtengo.
21. Alusira cumba wosabala,Osamcitira wamasiye cokoma.
22. Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yace;Iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.
23. Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;Koma maso ace ali pa njira zao.
24. Akwezeka; m'kamphindi kuti zi;Inde atsitsidwa, acotsedwa monga onse ena,Adutidwa ngati tirigu ngala zace.
25. Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndiri wabodza,Ndi kuyesa mau anga opanda pace?