5. Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga,Ndi citonthozo ca milomo yanga cikadatsitsa cisoni canu.
6. Cinkana ndinena cisoni canga sicitsika;Ndipo ndikaleka, cindicokera nciani?
7. Koma tsopano wandilemetsa Iye;Mwapasula msonkhano wanga wonse.
8. Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa,Kuonda kwanga kundiukira, kucita umboni pamaso panga.
9. Iye ananding'amba m'kundida kwace, nakwiya nane,Anandikukutira mano;Mdani wanga ananditong'olera maso ace.
10. Iwo anandiyasamira pakamwa pao;Anandiomba pama ndi kunditonza;Asonkhana pamodzi kunditsutsa.
11. Mulungu andipereka kwa osalungama,Nandiponya m'manja a oipa.
12. Ndinali mkupuma, koma anandityola;Inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya;Anandiimika ndikhale candamali.