9. Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,Nudzaswa nthambi ngati womera.
10. Koma munthu akufa atacita liondeondeInde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti?
11. Madzi acoka m'nyanja,Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;
12. Momwemo munthu agona pansi, osaukanso;Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,Kapena kuutsidwa pa tulo tace.
13. Ha! mukadandibisa kumanda,Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.
14. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,Mpaka kwafika kusandulika kwanga,
15. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;Mukadakhumba nchito ya manja anu.