Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi cofunkha ca woopsya cidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.