Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha ku mphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.