Cifukwa cace coipa cidzafika pa iwe; sudzadziwa kuca kwace, ndipo cionongeko cidzakugwera; sudzatha kucikankhira kumbali; ndipo cipasuko cosacidziwa iwe cidzakugwera mwadzidzidzi.