Yimbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wacicita ico; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; yimbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; cifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israyeli.