Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilume lao lilephera, cifukwa ca ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israyeli sindidzawasiya.