9. Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atacira nthenda yace.
10. Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.
11. Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;
12. Pokhala panga pacotsedwa, pandisunthikira monga hema wambusa;Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba;Iye adzandidula ine poomberapo;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.