3. Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndacita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.
4. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,
5. Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.
6. Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.