10. Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.
11. Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumarizani inu.
12. Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.
13. Imvani inu amene muli kutari, cimene ndacita ndi inuamene muli pafupi, bvomerezani mphamvu zanga,
14. Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?
15. Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;
16. iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.
17. Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.
18. Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?