Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Aigupto kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magareta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israyeli, ngakhale kumfuna Yehova!