Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; cifukwa cace inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; cifukwa cace iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.