16. Yehova, iwo adza kwa Inu mobvutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.
17. Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.
18. Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.
19. Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muyimbe, inu amene mukhala m'pfumbi; cifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzaturutsa mizimu.
20. Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.
21. Pakuti taonani, Yehova adza kucokera ku malo ace kudzazonda okhala pa dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao; dziko lidzabvumbulutsa mwazi wace, ndipo silidzabvundikiranso ophedwa ace.