Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosaceka, ndi dzanja lace lirikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'cigwa ca Refaimu.