Ndipo cikondwero ndi msangalalo zacotsedwa m'munda wapatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuyimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mpfuu wa masika amphesa.