4. Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lace, mulalikire macitidwe ace mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lace lakwezedwa.
5. Muyimbire Yehova; pakuti wacita zaulemerero; cidziwike ici m'dziko lonse.
6. Tapfuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, cifukwa Woyera wa Israyeli wa m'kati mwako ali wamkuru.