20. Cofukiza cindifumiranji ku Seba, ndi nzimbe ku dziko lakutari? nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.
21. Cifukwa cace atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zopunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzace adzatayika.
22. Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu ucokera kumpoto; ndi mtundu waukuru adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.
23. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.
24. Tamva ife mbiri yace; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.
25. Usaturukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.
26. Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udzibveke ndi ciguduli, ndi kubvimbvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.
27. Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.
28. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi citsulo; onsewa acita mobvunda;
29. mbvukuto yatenthedwa ndi moto; mthobvu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga cabe; pakuti oipa sacotsedwa.
30. Anthu adzawacha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.