Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.