Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ace, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakucita zolungama, wakufuna coonadi; ndipo ndidzamkhululukira.