9. Akafika kwa inu akuchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?
10. Pakuti ndambvula Esau, ndambvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zace zaonongeka, ndi abale ace, ndi anansi ace, ndipo palibe iye.
11. Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.
12. Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwa kuti amwe cikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.
13. Pakuti ndalumbira, Pali Ine, ati Yehova, kuti Boma adzakhala cizizwitso, citonzo, copasuka, ndi citemberero; ndipo midzi yace yonse idzakhala yopasuka cipasukire.