43. Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, ziri pa iwe, wokhala m'Moabu, ati Yehova.
44. Ndipo iye wakuthawa cifukwa ca mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Moabu, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.
45. Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pa mthunzi wa Hesiboni; pakuti moto waturuka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngondya ya Moabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso,
46. Tsoka iwe, Moabu! anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako amuna atengedwa ndende, ndi ana ako akazi atengedwa ndende.
47. Koma ndidzabwezanso undende wa Moabu masiku akumariza, ati Yehova. Ziweruzo za Moabu ndi zomwezi.