Palibenso kutamanda Moabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu waanthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.