Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Akasidi, amene adzadza kwa ife; koma inu, sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.