3. Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, ndipo adzaulanda.
4. Ndipo akuru anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; cifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.
5. Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kucita kanthu kotsutsana nanu.
6. Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wace wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe, Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.
7. Ndipo pamene Ebedi-Meleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu irikukhala pa cipata ca Benjamini;
8. Ebedi-Meleki anaturuka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,
9. Mbuyanga mfumu, anthu awa anacita zoipa m'zonse anacitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo cifukwa ca njala; pakuti mulibe cakudya cina m'mudzimu.