Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ngati mudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;