18. Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pace anandichulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m'bukumo.
19. Ndipo akuru anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.
20. Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m'cipinda ca Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m'makutu a mfumu.
21. Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.