Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo ku mudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.