41. Inde, ndidzasekerera iwo kuwacitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42. Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa coipa conseci, comweco ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonieza.
43. Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Akasidi.