Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Cifukwa canji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo iye adzaulanda,