Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israyeli; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzaturukira masewero a iwo akukondwerera.