Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.