Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, cifukwa ca lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.