Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; cifukwa ca Yehova, ndi cifukwa ca mau ace opatulika.