Titunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu wa ku Babulo atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzaticitira ife monga mwa nchito zace zolapitsa, kuti aticokere.