Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;