6. Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako;Pakuti cikondi cilimba ngati imfa;Njiru imangouma ngati manda:Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto,Ngati mphezi ya Yehova,
7. Madzi ambiri sangazimitse cikondi,Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola:Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yace ngati sintho la cikondi,Akanyozedwa ndithu.
8. Tiri ndi mlongwathu wamng'ono,Alibe maere;Ticitirenji mlongwathuTsiku lokhoma unkhoswe wace?
9. Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.
10. Ndine khoma, maere anga akunga nsanja zace:Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
11. Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni;Nabwereka alimi mundawo;Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.
12. Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu;Naco cikwico, Solomo iwe,Koma olima zipatso zace azilandira mazana awiri.