Ndaniyu acokera kucipululu,Alikutsamira bwenzi lace?Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:Pomwepo amako anali mkusauka nawe,Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.