Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakacitira Yehova Paskha, azicita monga mwa lemba la Paskha, ndi monga mwa ciweruzo cace; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.