7. azibvomereza cimo lace adalicita; nabwezere coparamulaco monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kucipereka kwa iye adamparamulayo.
8. Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere coparamulaco, coparamula acibwezera Yehovaco cikhale ca wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya cotetezerapo, imene amcitire nayo comtetezera.
9. Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zace.
10. Zopatulika za munthu ali yense ndi zace: ziti zonse munthu ali yense akapatsa wansembe, zasanduka zace.
11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
12. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wace, nakamcitira mosakhulupirika,
13. ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;
14. ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti acitire nsanje mkazi wace, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amcitire mkazi wace nsanje angakhale sanadetsedwa;
15. pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wace kwa wansembe, nadze naco copereka cace, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo libano; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yacikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.
16. Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;
17. natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko pfumbi liri pansi m'kacisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.