Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagona nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kucidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.